Joshua 22:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tidachita zimenezi chifukwa choopa kuti kutsogoloko zidzukulu zanu zingamadzanene zidzukulu zathu kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Aisraele, kodi inu muli naye nkanthu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ngati ife sitinachita ichi chifukwa cha kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli chiyani inu kwa Yehova Mulungu wa Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ayi! Ife tinachita izi kuopa kuti tsiku lina zidzukulu zanu zingadzanene kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Kodi inu mukufuna chiyani kwa Yehova Mulungu wa Israeli?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ngati ife sitinacita ici cifukwa ca kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli ciani inu kwa Yehova Mulungu wa Israyeli?