Joshua 22:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaika malire a Yordani pakati pa ife ndi inu, anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi. Motero, inu mulibe gawo mwa Chauta.’ Tsono mwina zidzukulu zanuzo nkudzaletsa zidzukulu zathu kupembedza Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova anaika Yordani ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anayika mtsinje wa Yorodani kukhala malire pakati pa ife ndi inu, anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi. Inuyo mulibe gawo mwa Yehova.’ Tsono mwina zidzukulu zanuzo nʼkudzaletsa zathu kupembedza Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti Yehova anaika Yordano ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope. Yehova.