Joshua 22:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma makamaka kuti chikhale chizindikiro pakati pa ife ndi inu. Ndipo chikhalenso chizindikiro kwa mibadwo yobwera pambuyo pathu, kuti idzadziŵe kuti timapembedzanso Chauta ndi nsembe zathu zopsereza, zopereka, ndiponso nsembe zamtendere. Motero zidzukulu zanu zisadzanene kwa zidzukulu zathu m'tsogolo muno kuti, ‘Inu mulibe gawo mwa Chauta.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu, ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikachita ntchito ya Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mosiyana ndi zimenezi, guwali likhale umboni pakati pa ife ndi inu ndiponso mibado imene ikubwerayo, kuti ife timapembedzanso Yehova ndi nsembe zathu zopsereza, zopereka, ndiponso nsembe za mtendere. Motero mʼtsogolo muno zidzukulu zanu sizidzatha kunena kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Inu mulibe gawo mwa Yehova!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu; ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikacita nchito ya Yehova pamaso pace ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.