Joshua 22:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneŵa ndiwo anali maganizo athu kuti, ngati zimenezi zidzachitika, ife tidzanene kuti, ‘Onani, makolo athu adamanga guwa lofanafana ndi guwa la Chauta. Limeneli silinali loperekerapo nsembe zopsereza kapena lopherapo nyama za nsembe, koma linali chizindikiro pakati pa ife ndi inu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m'tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, chitsanzo cha guwa la nsembe la Yehova, chomanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo ife tinati kuti, ‘Ngati iwo adzatiyankhulira kapena kuyankhulira zidzukulu zathu motero mʼtsogolo muno, ife tidzayankha kuti, onani guwa lansembe, lofanana ndi lomwe makolo athu anamanga osati loperekerapo nsembe zopsereza kapena nsembe zina koma ngati umboni pakati pa inu ndi ife.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m'tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, citsanzo ca guwa la nsembe la Yehova, comanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu.