Joshua 22:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sitingathe kupandukira Chauta. Sitingathenso kuleka kumtsata tsopano lino, ndi kumanga guwa la zopereka zopsereza, kapena chopereka cha chakudya kapenanso la nsembe zina, loti lizipikisana ndi guwa la Chauta wathu lomwe lili patsogolo pa malo opatulika m'mene Chauta amakhalamo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sikungatheke kuti tipikisane ndi Yehova ndi kubwerera lero kusatsata Yehova, kumanga guwa la nsembe la kufukizapo nsembe yopsereza, la nsembe yaufa, kapena yophera, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu lokhala pakhomo pa chihema chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Sizingatheke konse kuti ife lero nʼkupandukira Yehova. Ife sitingapatuke kuleka kumutsata Yehova ndi kumanga guwa lina la nsembe zopsereza, nsembe za zakudya, ndi nsembe zina zopikisana ndi guwa la Yehova, Mulungu wathu limene lili patsogolo pa Hema ya Yehova mʼmene amakhalamo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sikungatheke kuti tipikisane ndi Yehova ndi kubwerera lero kusatsata Yehova, kumanga guwa la nsembe la kufukizapo nsembe yopsereza, la nsembe yaufa, kapena yophera, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu lokhala pakhomo pa cihema cace.