Joshua 22:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe Finehasi ndi akuluakulu amene anali naye, amene anali atsogoleri a mabanja a Aisraele, atamva zimene adanena anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi la Manase, adakondwa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Finehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akulu a mabanja a Israele okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Finehasi wansembe ndi atsogoleri a gululo amene anali naye atamva zimene anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka lakummawa la fuko la Manase ananena, anakondwera kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Pinehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akuru a mabanja a Israyeli okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.