Joshua 22:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Finehasi, mwana wa wansembe Eleazara, adauza anthu a mafuko aja kuti, “Tsopano tadziŵadi kuti Chauta ali nafe, poti simudapanduke ndi kutsutsana ndi Chauta. Mwapulumutsa Aisraele ku chilango cha Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Finehasi, mwana wa Eleazara wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira nacho Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israele m'dzanja la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Finehasi wansembe, mwana wa Eliezara anati kwa mafuko a Rubeni, Gadi ndi Manase, “Lero tadziwa kuti Yehova ali nafe chifukwa zimene mwachitazi simunawukire nazo Yehova. Inu mwapulumutsa Aisraeli onse ku chilango cha Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Pinehasi, mwana wa Eleazare wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, Lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira naco Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israyeli m'dzanja la Yehova.