Joshua 22:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Finehasi, pamodzi ndi mafumuwo adachoka ku Giliyadi nasiya anthu a fuko la Rubeni pamodzi ndi la Gadi, nabwerera ku Kanani kwa Aisraele anzao, ndipo adakafotokoza zonsezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, ndi akalonga anabwerera kuchokera kwa ana a Rubeni, ndi kwa ana a Gadi, m'dziko la Giliyadi, kudza ku dziko la Kanani kwa ana a Israele, nawabwezera mau.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Finehasi mwana wa wansembe Eliezara, pamodzi ndi atsogoleriwo anachoka ku Giliyadi nasiya anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi nabwerera ku Kanaani kwa Aisraeli anzawo, ndipo anakafotokoza zonsezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Pinehasi mwana wa Eleazare wansembe, ndi akalonga anabwerera kucokera kwa ana a Rubeni, ndi kwa ana a Gadi, m'dziko la Gileadi, kudza ku dziko La Kanani kwa ana a Israyeli, nawabwezera mau.