Joshua 22:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano Chauta, Mulungu wanu, wapatsa mtendere Aisraele anzanu, monga momwe adaalonjezera. Motero bwererani kwanu ku dziko limene mudalandira, dziko limene lili patsidya pa mtsinje wa Yordani kuvuma, limene Mose mtumiki wa Chauta adakupatsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mukani ku mahema anu, ku dziko la cholowa chanu chimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono pakuti Yehova Mulungu wanu wapereka mpumulo kwa abale anu monga anayankhulira nawo, bwererani ku nyumba zanu ku dziko limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani, dziko limene lili pa tsidya la Yorodani kummawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mu kani ku mahema anu, ku dziko la colowa canu cimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordano.