Joshua 22:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musamale bwino kuti mumvere ndithu malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Mulungu adakupatsani. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zimene Iyeyo akufuna, muzimvera malamulo ake, muzikhala okhulupirika kwa Iye, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi mzimu wanu wonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma samalirani bwino kuti muchite chilangizo ndi chilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake zonse ndi kusunga malamulo ake, ndi kumuumirira Iye, ndi kumtumikira Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma samalitsani kuti mumvere malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani: kukonda Yehova Mulungu wanu, kuchita zimene iye amafuna, kumvera malamulo ake, kukhala okhulupirika kwa Iye ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma samalirani bwino kuti mucite cilangizo ndi cilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace zonse ndi kusunga malamulo ace, ndi kumuumirira iye, ndi kumtumikira iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.