Joshua 22:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose anali atapatsa theka lina la fuko la Manase ku dziko la Basani. Koma theka lina la fuko la Manase, Yoswa adalipatsa dziko kuzambwe kwa Yordani, pamodzi ndi abale ao onse. Pamene Yoswa ankaŵatumiza kwao anthu amenewo, adaŵadalitsa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo gawo limodzi la fuko la Manase, Mose anawapatsa cholowa m'Basani; koma gawo lina Yoswa anawaninkha cholowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordani kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apa nʼkuti Mose atapereka dziko la Basani ku theka lina la fuko la Manase. Koma theka lina la fuko la Manase Yoswa analipatsa dziko la kumadzulo kwa Yorodani pamodzi ndi abale awo onse. Pamene Yoswa ankawatumiza kwawo anthu amenewa, anawadalitsa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo gawo limodzi la pfuko la Manase, Mose anawapatsa colowa m'Basana; koma gawo lina Yoswa anawaninkha colowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordano kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;