Joshua 22:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
naŵauza kuti, “Tsopano mukubwerera kwanu mutalemera. Muli ndi ng'ombe zambiri, mulinso ndi siliva, golide, mkuŵa, zitsulo ndi zovala zambiri. Izi zimene mudafunkha kwa adani anu, mugaŵireko Aisraele anzanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena nao ndi kuti, Bwererani nacho chuma chambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndi siliva, ndi golide, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi malaya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nawawuza kuti, “Mukubwerera kwanu ndi chuma chambiri. Muli ndi ngʼombe zambiri pamodzi ndi siliva, golide, mkuwa ndi chitsulo, ndiponso zovala zambiri. Izi zimene munafunkha kwa adani anu agawireni abale anu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena nao ndi kuti, Bwererani naco cuma cambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndi siliva, ndi golidi, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi maraya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.