Joshua 22:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero anthu onse a fuko la Rubeni ndi la Gadi, pamodzi ndi theka lija la fuko la Manase, adabwerera kwao. Aisraele ena onse adaŵasiya ku Silo m'dziko la Kanani, ndipo iwowo adapita ku dziko la Giliyadi. Dziko limeneli ndilo linali lao, chifukwa adalilandira potsata malamulo a Chauta kudzera mwa Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mafuko a Rubeni, Gadi, pamodzi ndi theka la fuko la Manase anabwerera kwawo. Aisraeli ena onse anawasiya ku Silo mʼdziko la Kanaani. Tsono anapita ku dziko la Giliyadi, dziko limene linali lawo popeza analilandira potsata malamulo a Yehova kudzera mwa Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anabwerera, nacoka kwa ana a Israyeli ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kumka ku dziko la Gileadi, ku dziko lao lao, limene anakhala eni ace, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.