Joshua 23:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Padapita nthaŵi yaikulu chiyambire pamene Chauta adakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraele ndi adani ao oŵazungulira. Pamenepo nkuti Yoswa atatheratu nkukalamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israele kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panapita nthawi yayitali kuchokera pamene Yehova anakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraeli ndi adani awo owazungulira. Nthawi imeneyi nʼkuti Yoswa atakalamba, ali ndi zaka zambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israyeli kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri;