Joshua 23:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense mwa inu angathe kuthamangitsa anthu chikwi chimodzi, chifukwa Chauta ndiye akukumenyerani nkhondo monga adalonjezera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense wa inu atha kuthamangitsa anthu 1,000 chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye amakumenyerani nkhondo, monga momwe analonjezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu mmodzi wa inu adzapitikitsa anthu cikwi cimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.