Joshua 23:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, sadzapirikitsa mitundu imeneyi pamaso panu. Koma anthuwo adzakhala ngati msampha kwa inu, kapenanso ngati khwekhwe. Adzakhalanso ngati chikoti choŵaŵa pamsana panu, kapena ngati minga zokulasani m'maso mwanu. Zimenezi zidzachitikabe mpaka inuyo mutatha m'dziko labwinoli limene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo mudziwe kuti Yehova, Mulungu wanu, sadzapirikitsa mitundu imeneyi pamaso panu, koma idzakhala ngati msampha kwa inu kapenanso khwekhwe lokukolani. Idzakhala ngati zikwapu pa msana panu kapenanso ngati minga mʼmaso mwanu mpaka mutatha psiti mʼdziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.