Joshua 23:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine ndi ulendo uno tsopano. Aliyense mwa inu akudziŵa bwino lomwe mumtima mwake ndi mumzimu mwake kuti Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani zinthu zonse zabwino zimene adaalonjeza. Zonse zimene adaalonjeza, zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silidachitike.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, lero lino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwe padera mau amodzi; onse anachitikira inu, sanasowepo mau amodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aliyense wa inu akudziwa mu mtima mwake komanso mʼmoyo mwake kuti zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wanu anakulonjezani zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silinakwaniritsidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, lero lino ndirikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mau amodzi; onse anacitikira inu, sanasowapo mau amodzi.