Joshua 23:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe Chauta, Mulungu wanu, wakuchitirani zabwino zonse zimene adaanena kuti adzachita, choncho angathe kukuchitani zoipa, mpaka kukuchotsani m'dziko lokomali limene Iye adakupatsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukuchotsani m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe Yehova Mulungu wanu wakuchitirani zabwino zonse zimene ananena kuti adzachita, Yehovayo angathenso kukuchitirani zoyipa zonse zimene waopseza, mpaka kukuchotsani mʼdziko lokoma limene anakupatsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukucotsani m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.