Joshua 23:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati simusunga chipangano chomwe Chauta adakulamulani, mukamapita kukatumikira milungu ina ndi kumakaigwadira, Chauta adzakupserani mtima, ndipo sipadzatsala ndi mmodzi yense m'dziko labwino limene adakupatsanilo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukalakwira chipangano cha Yehova Mulungu wanu chimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m'dziko lokomali anakupatsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati muphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu, limene anakulamulirani nʼkumapita kukatumikira milungu ina ndi kuyigwadira, Yehova adzakukwiyirani, ndiye mudzachotsedwa mʼdziko labwinoli limene Yehova wakupatsani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukalakwira cipangano ca Yehova Mulungu wanu cimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu yina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m'dziko lokomali anakupatsani.