Joshua 23:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yoswayo adaitana Aisraele onse, pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao a anthuwo, naŵauza kuti “Tsopano ine ndakalamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yoswa anaitana Aisraele onse, akuluakulu ao, ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswayo anayitanitsa Aisraeli onse pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, oweruza, ndi oyangʼanira anthu antchito ndipo anawawuza kuti, “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yoswa anaitana Aisrayeli onse, akulu akulu ao, ndi akuru ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;