Joshua 23:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonse zimene Chauta wachitira mitundu ina yonseyi chifukwa cha inu, mwazipenya. Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene wakumenyerani nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anachitira mitundu iyi yonse ya anthu chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachita kwa mitundu yonseyi chifukwa cha inu. Ndi Yehova Mulungu wanu amene anakumenyerani nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anacitira mitundu iyi yonse ya anthu cifukwa ca inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.