Joshua 23:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzaŵathaŵitse pamaso panu. Inuyo mudzatenga maiko ao monga momwe Chauta, Mulungu wanu, wakulonjezerani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapirikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwachotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale cholowa chanu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wanu ndiye adzawathamangitsa pamaso panu. Mudzatenga dziko lawo monga Yehova anakulonjezerani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapitikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwacotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale colowa canu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.