Joshua 24:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudaoloka Yordani ndi kufika ku Yeriko. Anthu a ku Yeriko adalimbana nanu, kudzanso Aamori, Aperizi, Akanani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi. Ine ndidaŵapereka m'manja mwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo munaoloka Yordani, ndi kufika ku Yeriko; ndi eni ake a ku Yeriko anaponyana nanu nkhondo, Aamori, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahiti, ndi Agirigasi, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ndipo inu munawoloka Yorodani ndi kufika ku Yeriko. Anthu a ku Yeriko analimbana nanu pamodzi ndi Aamori, Aperezi, Akanaani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi. Koma Ine ndinawapereka mʼdzanja lanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo munaoloka Yordano, ndi kufika ku Yeriko; ndi eni ace a ku Yeriko anaponyana nanu nkhondo, Aamori, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahiti, ndi Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu.