Joshua 24:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakupatsani dziko limene inuyo simudaligwirire ntchito, pamodzi ndi mizinda imene simudaimange. Mukukhala kumeneko ndi kumangodya mphesa ndi olivi, zimene inu simudabzale.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinakupatsani dziko limene simunagwiramo ntchito, ndi midzi simunaimanga, ndipo mukhala m'mwemo; mukudya za m'minda yamphesa, ndi minda ya azitona imene simunaioka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero ndinakupatsani dziko limene simunalivutikire ndiponso mizinda imene simunamange. Inu mukukhala mʼmenemo ndi kumadya zipatso za mʼmunda wamphesa ndi kuthyola zipatso mʼmitengo ya olivi zimene simunadzale.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinakupatsani dziko limene simunagwiramo nchito, ndi midzi simunaimanga, ndipo mukhala m'mwemo; mukudya za m'minda yamphesa, ndi minda yaazitona imene simunaioka.