Joshua 24:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adauza anthu onsewo kuti, “Zimene Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena ndi izi, akuti, ‘Kale makolo anu ankakhala pa mbali ina ya mtsinje wa Yufurate, ndi kumapembedza milungu ina. Mmodzi mwa makolo ameneŵa anali Tera, bambo wa Abrahamu ndi Nahori.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa anati kwa anthu onse, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Kalekale makolo anu, kuphatikiza Tera, abambo a Abrahamu ndi Nahori ankakhala kutsidya kwa Mtsinje ndipo ankapembedza milungu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu yina iwowa.