Joshua 24:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukasiya Chauta, Mulungu wanu, ndi kumakatumikiranso milungu yachilendo, adzakufulatirani, ndipo adzakulangani. Adzakuwonongani ngakhale kuti kale adakuchitirani zabwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukasiya Yehova, ndi kutumikira milungu yachilendo, adzatembenuka ndi kukuchitirani choipa, ndi kukuthani, angakhale anakuchitirani chokoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati inu musiya Yehova ndi kutumikira milungu yachilendo, adzakufulatirani. Iye adzakulangani ndi kukuwonongani ngakhale kuti poyamba anakuchitirani zabwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukasiya Yehova, ndi kutumikira milungu yacilendo, adzatembenuka ndi kukucitirani coipa, ndi kukuthani, angakhale anakucitirani cokoma.