Joshua 24:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abrahamuyo ndidamtenga ndi kumchotsa m'dzikomo patsidya pa Yufurate, ndipo ndidamtsogoza kupita naye ku dziko la Kanani. Ndidampatsa zidzukulu zambiri. Ndidampatsa Isaki,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m'dziko lonse la Kanani ndi kuchulukitsa mbeu zake ndi kumpatsa Isaki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ine ndinatenga kholo lanu Abrahamu kumuchotsa ku dziko la kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate ndipo ndinamutsogolera kupita ku dziko la Kanaani. Ndinamupatsa zidzukulu zambiri. Ndinamupatsa Isake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m'dziko lonse la Kanani ndi kucurukitsa mbeu zace ndi kumpatsa Isake,