Joshua 24:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adatumikira Chauta pa nthaŵi yonse ya moyo wa Yoswa ndiponso pa nthaŵi ya atsogoleri amene adakhala ndi moyo Yoswa atafa. Atsogoleriwo adadziŵa ntchito zonse zimene Chauta adachitira Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Israele anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene anadziwa ntchito yonse ya Yehova anaichitira Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Israeli anatumikira Yehova pa nthawi yonse imene Yoswa anali ndi moyo ndiponso pa nthawi ya akuluakulu amene anali moyo Yoswa atamwalira, anthu amene ankadziwa zonse zimene Yehova anachitira Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Israyeli anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akulu akulu otsala atafa Yoswa, amene anadziwa nchito yonse ya Yehova anaicitira Israyeli.