Joshua 24:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafupa a Yosefe amene Aisraele adaŵatenga ku Ejipito, adakaŵaika ku Sekemu m'kadziko kamene Yakobe adaagula kwa ana a Hamori, bambo wa Sekemu, pa mtengo wa ndalama zasiliva zana limodzi. Ndipo dzikolo lidasanduka choloŵa cha zidzukulu za Yosefe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israele anakwera nao kuchokera ku Ejipito anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mafupa a Yosefe amene Aisraeli anawatulutsa ku Igupto anawayika mʼmanda a ku Sekemu pa malo amene Yakobo anagula ndi ndalama zasiliva 100 kwa ana a Hamori, abambo a Sekemu. Malo awa anakhala cholowa cha adzukulu a Yosefe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israyeli anakwera nao kucokera ku Aigupto anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala colowa ca ana a Yosefe.