Joshua 24:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo Isakiyo ndidampatsa Yakobe ndi Esau. Dziko lamapiri la Seiri ndidapatsa Esau kuti likhale choloŵa chake, koma Yakobe ndi ana ake adatsikira ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Isake ndinamupatsa Yakobo ndi Esau. Ndinapereka dziko la mapiri la Seiri kwa Esau, koma Yakobo ndi ana ake anapita ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kwa Isake ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lace lace; koma Yakobo ndi ana ace anatsikira kumka ku Aigupto.