Joshua 24:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo ndidatuma Mose ndi Aroni ku Ejipitoko, ndipo ndidazunza kwambiri Aejipitowo. Pambuyo pake ndidakutulutsani inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aejipito, monga ndinachita pakati pake; ndipo nditatero ndinakutulutsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Kenaka ndinatuma Mose ndi Aaroni, ndipo ine ndinazunza Aigupto. Pambuyo pake ndinakutulutsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aigupto, monga ndinacita pakati pace; ndipo nditatero ndinakuturutsani.