Joshua 24:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makolo anuwo atapemphera mokhulupirira kwa Ine, ndidaika mtambo wakuda pakati pa iwo ndi Aejipitowo, ndipo nyanja idaŵamiza Aejipito onsewo. Mudapenya ndi maso anu zomwe ndidachita Ejipito, ndipo mudakhala nthaŵi yaitali m'chipululu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine m'Ejipito; ndipo munakhala m'chipululu masiku ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono makolo anuwo anapemphera kwa Ine kuti ndiwathandize, ndipo ndinayika mtambo wakuda pakati pawo ndi Aiguptowo, ndipo Nyanja inamiza Aigupto aja. Inu munaona ndi maso anu zimene ndinachita kwa Aiguptowo ndipo inu munakhala mʼchipululu nthawi yayitali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anapfuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aaigupto nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya cocita Ine m'Aigupto; ndipo munakhala m'cipululu masiku ambiri.