Joshua 24:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“ ‘Pambuyo pake Ine ndidakufikitsani ku dziko la Aamori, amene ankakhala kuvuma kwa mtsinje wa Yordani. Adalimbana nanu iwowo, koma Ine ndidaŵapereka m'manja mwanu, mwakuti mudalanda dziko lao, chifukwa Ine ndidaŵaononga inu mukufika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinakulowetsani inu m'dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordani; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanulanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pambuyo pake Ine ndinabwera nanu ku dziko la Aamori amene amakhala kummawa kwa Yorodani. Iwo anamenyana nanu koma ndinawapereka mʼdzanja lanu. Ndinawawononga pamaso panu, ndipo inu munalanda dziko lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinakulowetsani inu m'dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordano; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanu lanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu.