Joshua 24:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Amowabu, adalimbana ndi Israele. Iyeyu adatumiza mau kwa Balamu mwana wa Beori, nampempha kuti akutemberereni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, anauka naponyana ndi Israele; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, analimbana ndi Israeli. Iye anayitanitsa Balaamu mwana wa Beori kuti akutemberereni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Moabu, anauka naponyana ndi Israyeli; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu;