Joshua 3:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'mamaŵa kutacha Yoswa adanyamuka. Iye, pamodzi ndi Aisraele onse, adatuluka ku Sitimu kuja, napita ku Yordani, ndipo adagona kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kuchoka ku Sitimu, nafika ku Yordani, iye ndi ana onse a Israele; nagona komweko, asanaoloke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa ndi Aisraeli onse anadzuka mmamawa nanyamuka ku Sitimu kupita ku Yorodani. Iwo anagona kumeneko asanawoloke mtsinje wa Yorodaniwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kucoka ku Sitimu, nafika ku Yordano, iye ndi ana onse a Israyeli; nagona komweko, asanaoloke.