Joshua 3:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
madzi onse adaima osayendanso. Madzi akumtunda adaundana ngati khoma lalitali, kuchokera ku Adama mpaka ku mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ndiye kuti Nyanja Yakufa, adatheratu pamalopo, ndipo anthu adaolokera tsidya lina, pafupi ndi Yeriko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mudzi wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
madzi ochokera ku mtunda anasiya kuyenda. Madzi a Yorodani ochokera ku mtunda anawunjikana pamodzi ngati khoma lalitali pa mtunda wautali ndithu ndi mzinda wa Adama chapafupi ndi mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ngakhalenso amene amachokera kuti Nyanja ya Mchere amathera pamenepo. Choncho anthu anawoloka tsidya lina moyangʼanana ndi Yeriko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo madzi ocokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adamu, ndiwo mudzi wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kumka ku nyanja ya cidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.