Joshua 3:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chonsecho nkuti ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja ataima pakatimpakati pa mtsinje wa Yordani uja, mpaka anthu onse adatha kuwoloka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anali chiyimire powuma, pakati pa Yorodani pamene Aisraeli amawoloka mpaka gulu lonse linamaliza kuwoloka powuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ansembe akulisenza likasa la cipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordano, ndi Aisrayeli onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordano.