Joshua 3:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Potero mudzaidziŵa njira yoyenera kutsata, popeza kuti nkale lomwe kumeneko simudadzereko. Komatu tsono Bokosi lachipanganolo musaliyandikire. Pakati pa inu ndi Bokosilo pazikhala mtunda wosachepera kilomita imodzi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapita njirayi kufikira lero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Potero mudzadziwa njira yoti mudzere, popeza simunayendepo njira ino nʼkale lomwe. Koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi bokosilo pakhale mtunda pafupifupi kilomita imodzi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapita njirayi kufikira lero.