Joshua 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Chauta adauza Yoswa kuti, “Zimene ndikuchita lerozi, ndizo zidzapatse Aisraele onse mtima wokulemekeza iwe, kuti ndiwe munthu wamkulu. Ndipo adzadziŵa kuti Ine ndili nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Lero Ine ndidzayamba kukukweza pamaso pa Aisraeli onse kuti adziwe kuti ndili nawe monga ndinalili ndi Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisrayeli onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.