Joshua 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe amene akunyamula Bokosi lachipangano la Chauta, uŵalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yordani, muloŵe m'madzimo ndi kuima m'mphepete.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima m'Yordani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe amene akunyamula Bokosi la Chipangano uwalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yorodani mulowe mu mtsinjemo ndi kuyima mʼmphepete.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la cipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordano muziima m'Yordano.