Joshua 4:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe aja adaimirirabe pakati pa mtsinje wa Yordani, mpaka zitatha zonse zimene Chauta adaalamula Yoswa kuti auze anthu. Zimenezi ndizo zimene Mose anali atafotokozera Yoswa. Tsono anthu adaoloka mtsinjewo mofulumira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordani, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe onyamula Bokosi lija anayimirirabe pakati pa Yorodani mpaka zonse zimene Yehova analamulira Yoswa kuti awuze anthu zinatha. Zimenezi zinali monga momwe Mose anamufotokozera Yoswa. Tsono anthu anawoloka mtsinjewo mofulumira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordano, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.