Joshua 4:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi theka la Manase, ndiwo adaoloka poyamba, ali okonzekera nkhondo, monga momwe Mose adaŵauzira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi gawo lija la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase anawoloka patsogolo pa Aisraeli ali ndi zida, monga momwe Mose anawalamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi gawo lija la pfuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israyeli, monga Mose adanena nao;