Joshua 4:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene adachita Chauta pa tsiku limenelo zidapatsa anthu mtima wolemekeza Yoswa. Ndipo adamchitira ulemu kwambiri ndi kumlemekeza monga momwe ankalemekezera Mose nthaŵi yonse ya moyo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisraele onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse a moyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimene Yehova anachita tsiku limeneli zinapatsa anthu mtima wolemekeza Yoswa. Ndipo anamulemekeza masiku onse a moyo wake, monga momwe analemekezera Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisrayeli onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse amoyowace.