Joshua 4:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adaoloka mtsinje wa Yordani tsiku lakhumi la mwezi woyamba, ndipo adamanga zithando zao ku Giligala, kuvuma kwa Yeriko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anakwera kutuluka m'Yordani tsiku lakhumi la mwezi woyamba, namanga misasa ku Giligala, mbali ya ku m'mawa kwa Yeriko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anawoloka Yorodani tsiku lakhumi la mwezi woyamba ndipo anakamanga misasa yawo ku Giligala mbali ya kummawa kwa Yeriko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anakwera kuturuka m'Yordano tsiku lakhumi la mwezi woyamba, namanga misasa ku Giligala, mbali ya ku m'mawa kwa Yeriko.