Joshua 4:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
muzidzaŵauza kuti, ‘Madzi a Yordani adaaima osayendanso, pamene Bokosi lachipangano la Chauta linkaoloka mtsinjewu.’ Miyala imeneyi idzakhala chikumbutso kwa Aisraele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzidzawawuza kuti, ‘Madzi a Yorodani analeka kuyenda pamene Bokosi la Chipangano la Yehova linkawoloka mtsinjewo. Miyala iyi idzakhala chikumbutso kwa anthu a Israeli kwa muyaya.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
munene nao, Cifukwa madzi a Yordano anadulidwa patsogolo pa likasa la cipangano ca Yehova; muja lidaoloka Yordano, madzi a Yordano anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala cikumbutso ca ana a Israyeli cikhalire.