Joshua 4:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adachitadi zonse zimene Yoswa adaŵalamula. Adanyamula miyala khumi ndi iŵiri pakati pa mtsinje wa Yordani, monga momwe Chauta adalamulira Yoswa. Anthu a fuko lililonse la Aisraele adanyamula mwala umodzi. Miyalayo adapita nayo kukaikhazika pansi pamalo pamene panali zithando paja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anachita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele; ndipo anaoloka nayo kunka kogona, naiika komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anachitadi monga Yoswa anawalamulira. Iwo ananyamula miyala khumi ndi iwiri kuchokera pakati pa Yorodani, fuko lililonse la Israeli mwala wake, monga Yehova analamulira Yoswa. Miyalayo anapita nayo ku misasa yawo nakayikhazika kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anacita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordano, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mapfuko a ana a Israyeli; ndipo anaoloka nayo kumka kogona, naiika komweko.