Joshua 4:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoswa adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri imene idaali pakati pa mtsinje wa Yordani, pamalo pomwe padaaimirira ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja. Miyala imeneyi ikadali kumeneko mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoswa anayimika miyala khumi ndi iwiri imene inali pakati pa Yorodani pamalo pamene ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anayimapo. Ndipo miyalayo ili pamalo pomwepo mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordano, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la cipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.