Joshua 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafumu onse a Aamori amene ankakhala kuzambwe kwa Yordani, pamodzi ndi mafumu a Akanani okhala m'mphepete mwa nyanja, adamva kuti Chauta adaumitsa Yordani pamene Aisraele ankaoloka. Choncho adachita mantha, ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraelewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafumu onse a Aamori, a kummawa kwa Yorodani ndi mafumu onse a Akanaani a mʼmbali mwa Nyanja anamva momwe Yehova anawumitsira Yorodani pamene Aisraeli ankawoloka. Choncho anachita mantha ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraeliwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordano, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku Nyanja ya Mcere anamvakuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordano pamaso pa ana a Israyeli mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo cifukwa ca ana a Israyeli.