Joshua 5:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake mpamene anthu aja adayamba kudya chakudya cha ku Kanani. Adakazinga tirigu, naphikanso buledi wosatupitsa tsiku limenelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mawa mwake atatha Paska, anadya tirigu wakhwimbi wa m'dziko, mikate yopanda chotupitsa ndi tirigu wokazinga tsiku lomwe lija.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake ndi pamene anayamba kudya zakudya za mʼdziko la Kanaani. Anaphika buledi wopanda yisiti ndi kukazinga tirigu tsiku lomwelo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mawa mwace atatha Paskha, anadya tirigu wakhwimbi wa m'dziko, mikate yopanda cotupitsa ndi tirigu wokazinga tsiku lomwe lija.