Joshua 5:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitangotero, mana uja adaleka kugwa, ndipo sadapezekenso pakati pa Aisraele. Kuyambira nthaŵi imeneyo adayamba kudya chakudya cha ku Kanani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma m'mawa mwake mana analeka, atadya iwo tirigu wakhwimbi wa m'dziko; ndipo ana a Israele analibenso mana; koma anadya zipatso za dziko la Kanani chaka chomwe chija.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atangodya chakudya cha mʼdzikomo, mana anasiya kugwa, ndipo sanapezekenso. Kuyambira nthawi imeneyo Aisraeli anayamba kudya chakudya cha mʼdziko la Kanaani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma m'mawa mwace mana analeka, atadya iwo tirigu wakhwimbi wa m'dziko; ndipo ana a Israyeli analibenso mana; koma anadya zipatso za dziko la Kanani caka comwe cija.